NJIRA ZOTETEZERA ANA KUNKHAZA ZOGONANA NDI KU GWIRIRIDWA

NJIRA ZOTETEZERA ANA KUNKHAZA ZOGONANA NDI KU GWIRIRIDWA

NJIRA ZOTETEZERA ANA KUNKHAZA ZOGONANA NDI KU GWIRIRIDWA

M’chaka cha 2023 chinali ndizambiri zomvesa chisoni monga kungwa kwa mvula yaukali yomwe adapha anthu ambiri komaso tinamaliza ndi kuva nkhani ya abusa ena ku Mangochi omwe adapezeka wolakwa pa mlandu wongwirira mwana wake komaso tidava nkhani ya mtsikana wina amene adamphedwa mboma la Thyolo ndi azibambo ena amene adamungwiririra. 


Ife ngati bungu tikuthokoza mtsogolereri wanthu wakele bambo Maxwell Matewere amene walora kuti kuyambira mchaka chino cha 2024 tingawe mwaulele Buku lomwe adalemba lomphunzitsa anthu za njira zotetezera ana kunkhaza zogonana ndi ku ngwiriridwa.

 
ZA MKATI MWA BUKU 
Ana amakumana ndi nkhanza zosiyanasiyana zomwe zimabweretsa manzunzo aakulu komanso kuphedwa kumene pofuna kubisa umboni. Pachifukwa cha ichi, ife mbuyomu tinayambitsa ntchito zosiyanasiyana zomwe cholinga chake ndi kudziwitsa anthu za nkhanza zomwe ana amakumana nazo monga kuthetsa maukwati a ana, kuzembaitsidwa, kuchotsedwa ziwalo komanso kugwiritsidwa ntchito zoposa msinkhu wawo mwazina. 


Nkhanza zambirizi zimachitika m’manyumba, m’mabanja, m’madera, m’malo opempherera, m’msukulu, malo osamalira ana a masiye, m’minda ya tiyi ndi fodya, komanso m’malo omwe ana akugwira ntchito za m’nyumba maka m’mizinda. 
Bukuli likukamba za nkhanza zogonana ndi ana. Bukuli likutsindika zomwe tikuyenera kuchita kuti tipewe komanso kuteteza ana ku mchitidwe wosayenerawu womwe wakhala ukuchuluka mu dziko muno.


Kuteteza ana ku nkhanza zakuthupi komanso kupusitsidwa ndi gawo lalikulu la ntchito yoteteza ana kubungwe la Eye of the Child (www.eyeofthechild.org).


Takhala tikuchirimika pothetsa nkhanzazi podziwitsa, pophunzitsa, pochita kafukufuku komanso potengapo gawo polemba malamulo othandiza kuteteza ana ku nkhanzazi. Tili okondwa ndi kusintha kwa lamulo la likulu la dziko lino la Konsititushoni, lamulo la Penal Code komanso kuyamba kugwira ntchito kwa lamulo loteteza ana la Child Care, Protection and Justice Act (2010)  zomwe zakhwimitsa chitetezo cha ana komanso kupereka zilango zokhwimwa kwa ochitira nkhanza ana. 


Komabe izo zilichocho ndizachidziwikire kuti ingakhale malamulo alipo, ndipofunika kudziwitsa anthu za malamulowa. Chofunika kwambiri ndi chakuti, makolo ndi ana akuyenera kudziwa za gawo komanso udindo wawo poteteza ufulu wa ana nthawi zonse.


Bukuli lidalembedwa kuti tidziwitse makolo m’mene nkhanza zogonana zimachitikira komanso m’mene zimakhudzira ana. Nkhanza zogonana ndi imodzi mwa nkhanza zomwe ana amakumana nazo kwambiri ndipo zimachitika mu zikhalidwe zosiyanasiyana zomwe zimabweretsa zovuta panthawi yayitali ku thupi ndi kumalingaliro a mwana.


Pali nkhani zambiri zomwe ana amanena zokhudza nkhanza zogonana zomwe zimasonyeza m’mene ana amamvetsetsera nkhaniza ufulu wawo komanso zomwe amaziona ngati ziphinjo pa ufulu wawo. Nkhani yaikulu ndiyakuti m’makomo ambiri komanso anthu akuluakulu akulephera kupanga malo otetezedwa komanso abwino oti ana adzikula mwa ufulu komanso kuti adzakhale nzika zodalirika.


Tikudziwa kuti ntchito yopanga malo oteteza ana ili pa mtima pa boma, makolo ambiri komanso ma bungwe. Pali zambiri zomwe zikuchitika kuti ana akhale ndi moyo wa bwino pa dziko lonse. Ndondomeko ndi ntchito zambiri zakhazikitsidwa kuti zithandize kuteteza ana. Ngakhale izi zili chonchi, ana sakukhalabe mu dziko lomwe amalota. Iwo akupitirira kukhala moyo wonyozeka, ndipo choyipa kwambiri, amachitiridwa nkhanza zogonana ndi anthu omwewo omwe akuyenera kuwasamalira ndi kuwateteza.


Bukuli lili ndi nkhani zoopsa zokhudza nkhanza zogwirira ndi zogonana kwa ana zomwe mtsogoleri wathu adathandiza pa nthawi yomwe amagwira ntchito yoteteza ana kuno kubungwe la Eye of the Child komanso zo chitika kumabwalo oweluza milandu.


Mwazina, nkhanizi zikufanana kwambiri kumbali yamomwe zinayendetsedwela ndi chithandizo chabwino chomwe chidapelekedwa pa milandu yokhudza nkhanza zogonana ndi ana; m’mene oganiziridwa milanduyi anamangidwira; komanso m’mene anazengedwera milandu ndi kulandira zilango.


Kubweretsa chidziwitso pa nkhanizi kutha kuthandiza makolo kuti amvetse m’mene nkhanza zogwirira komaso zogonana ndi ana zimachitikira, m’mene zingapewedwere, komanso zoti achite nkhanzazi zikachitika. Owelenga athanso kudziwa zomwe angachite kuti achepetse nkhanza zogonana kwa ana.


Mubukuli wolemnba adaunikiranso m’mene ntchito zokhwimitsa malamulo zimalepherera kuteteza ana chifukwa makolo samadziwa zoyenera kuchita ngati mwana wachitiridwa nkhanza zogonana kapena wina waonapo mwayi wopanga Ndalama pobisa chilungamo.
Kudzela maphunzilo ali Bukuli ndi cholinga chathu kubweretsa kusintha pa moyo wa mwana yemwe wachitiridwa nkhanza zogonana chifukwa zotsatira za kusachitapo kanthu ngati dziko zimakhala zoopsa kuziganizira. Mwazina ana omwe achitiridwa nkhaza zogonana amasiyira sukulu pa njira, amatenga matenda komanso ena amakhala amayi nthawi yawo isanakwane.


Bukuli muliso nkhani zomvetsa chisoni zomwe amayi anatengapo gawo lolimbikitsa kuti ana awo azigwiriridwa pofuna kusunga banja lawo. Pali milandu yambiri yomwe ana anagwiriridwa ndi abambo owapeza.


Atsikana amenewa amakakamizidwa kuchotsa mimba, nthawi zovutitsitsa, amagwiritsa ntchito mankhwala a zitsamba. Ena amathamangitsidwa kuti akakhale ndi agogo kumudzi komwe iwo ndi ana obadwa kuchokera ku nkhanzazi amasowa chisamaliro. 
Tamvapo za nkhani zomwe abambo amagwirira ana awo omwe atauzidwa ndi asing’anga kuti ndi kuteleko chizimba chopezera chuma.
Bukuli muwelenga momwe Makolo ena anali ndi kuthekera koteteza ana koma chifukwa cha kunyalanyaza anapereka mwayi woti ana awo achitiridwe nkhanza. Iwo sanazindikire mwachangu zizindikiro kapena ziopsezo ndipo ana awo anavutika kumapeto.


Palinso amayi ena omwe amachedwa kudziwitsa a polisi komanso pali a polisi ena omwe amanyalanyaza kuchitapo kanthu akalandira madandaulo otere posatsatira ndondomeko ndipo ana ochitiridwa nkhanza salandira thandizo.


Palinso atsikana ena omwe atenga matenda opatsirana pogonana kuphatikizapo ka chilombo koyambitsa matenda a Edzi kapena kutenga mimba, kukakamizidwa kubereka nthawi yawo isanakwane. Ena mwa iwo anayamba matenda a kadza mkodzo ndipo anasiyira sukulu pa njira. 


Bukuli lili ndi nkhani zokhudza amayi komaso abambo omwe amangidwa ndi kutsekeredwa ku ndende kamba ka mchitidwe ozunza ana zomwe tikukhulupira kuti zingameme komanso kudzetsa mkwiyo pakati pa anthu komaso makolo akufuna kwabwino kuti nkhanza zogonana ndi ana maka ana a akazi zichepe mchaka cha 2024.


Tiyeni kuyambira mchaka cha 2024 tipange madera athu kuti akhale malo omwe ana athu, maka a sungwana azimva kuti ndi otetezedwa komanso atha kukhulupilira anthu a akulu. 


Tonse tikumbutsidwe kuti tili ndi udindo woteteza ufulu wa ana ndipo tipange malo omwe angalole ana kuti akule ndikukhala anthu a chikondi omwe adzathe kusamalira ana awo. Tikumbukirenso kuti zomwe zimachitikira ana lero zidzakhudza momwe adzasamalire ana awo mtsogolo.


Bukuli mutha kulipeza pa website la bungwe lanthu la Eye of the Child – www.eyeothechild.org  
PLEASE SHARE THE MESSAGE KUTI TITHANE NAYE YENSE WOIPAYO 

Tobwanyani Pano kuti Mupeze Bukuli

 

Related Articles

“BETRAYAL OF TRUST” BOOK

“BETRAYAL OF TRUST” BOOK